Salimo 116:1-19
116 Ndimakonda YehovaChifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+
2 Amatchera khutu lake nʼkundimvetsera,*+Ndipo ndidzaitanira pa iye moyo wanga wonse.*
3 Zingwe za imfa zinandikulunga.Ndinkangomva ngati ndatsala pangʼono kufa.+
Ndinavutika chifukwa cha nkhawa komanso chisoni.+
4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+
“Inu Yehova, ndipulumutseni!”
5 Yehova ndi wokoma mtima* komanso wolungama.+Mulungu wathu ndi wachifundo.+
6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+
Ndinafooka chifukwa cha nkhawa koma iye anandipulumutsa.
7 Moyo wanga upumulenso,Chifukwa Yehova wandichitira zinthu mokoma mtima.
8 Inu mwandipulumutsa ku imfa,Mwapukuta misozi yanga ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe.+
9 Ndidzayenda pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ndinali ndi chikhulupiriro, nʼchifukwa chake ndinalankhula.+Ndinavutika kwambiri.
11 Nditapanikizika ndinati:
“Munthu aliyense ndi wabodza.”+
12 Yehova ndidzamubwezera chiyaniPa zabwino zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso,*Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,Pamaso pa anthu ake onse.+
15 Mʼmaso mwa YehovaImfa ya anthu ake okhulupirika ndi yopweteka kwambiri.*+
16 Ndikukupemphani, inu Yehova,Chifukwa ine ndi mtumiki wanu.
Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.
Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+
17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse,+
19 Mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,+Pakati pa iwe Yerusalemu.
Tamandani Ya!*+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “amawerama kuti andimvetsere.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku anga.”
^ Kapena kuti, “ndi wachisomo.”
^ Kapena kuti, “yachipulumutso chachikulu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nkhani yaikulu.”
^ Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.