Salimo 117:1, 2

  • Anthu a mitundu yonse akupemphedwa kuti atamande Yehova

    • Chikondi chokhulupirika cha Mulungu nʼchachikulu (2)

117  Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu.+Mulemekezeni, inu anthu a mitundu yonse.*+   Chifukwa chikondi chokhulupirika chimene amatisonyeza ndi chachikulu.+Kukhulupirika+ kwa Yehova kudzakhalapo mpaka kalekale.+ Tamandani Ya!*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “a mafuko onse.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.