Salimo 12:1-8

  • Yehova amanyamuka nʼkuchitapo kanthu

    • Mawu a Mulungu ndi oyera (6)

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide. 12  Ndipulumutseni, inu Yehova, chifukwa anthu okhulupirika atha.Anthu okhulupirika atheratu pakati pa anthu.   Iwo amauzana zinthu zabodza.Ndi milomo yawo, amayamikira ena mwachiphamaso* komanso kulankhula ndi mtima wachinyengo.*+   Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengoKomanso lilime lolankhula modzikweza.+   Iye adzadula anthu amene amanena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana. Timagwiritsa ntchito milomo yathu mmene tikufunira.Ndi ndani angatilamulire?”+   Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti ovutika akuponderezedwaChifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+Ndidzanyamuka nʼkuchitapo kanthu, Ndidzawapulumutsa kwa anthu amene akuwanyoza.”*   Mawu a Yehova ndi oyera.+Ali ngati siliva woyengedwa mungʼanjo yadothi nthawi zokwanira 7.   Inu Yehova mudzawayangʼanira.+Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.   Anthu oipa akungoyendayenda popanda wowaletsa,Chifukwa chakuti ana a anthu amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zoipa.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amalankhula ndi mlomo woshashalika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mtima komanso mtima.”
Kapena kuti, “akuwanyogodola.”