Salimo 120:1-7

  • Mlendo akulakalaka mtendere

    • ‘Ndipulumutseni ku lilime lachinyengo’ (2)

    • “Ine ndimakonda mtendere” (7)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.* 120  Nditakumana ndi mavuto ndinafuulira Yehova,+Ndipo iye anandiyankha.+  2  Inu Yehova, ndipulumutseni ku milomo yonamaKomanso ku lilime lachinyengo.  3  Iwe lilime lachinyengo,+Kodi Mulungu adzakuchitira chiyani ndipo adzakupatsa chilango chotani?*  4  Adzakulanga pogwiritsa ntchito mivi yakuthwa+ ya msilikaliKomanso makala amoto+ a mtengo wamʼchipululu.  5  Tsoka kwa ine, chifukwa ndakhala mʼdziko la Meseki+ ngati mlendo. Ndimakhala mutenti pakati pa matenti a ku Kedara.+  6  Ndakhala kwa nthawi yaitaliLimodzi ndi anthu odana ndi mtendere.+  7  Ine ndimakonda mtendere, koma ndikalankhulaIwo amafuna nkhondo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo kodi Iye adzawonjezera chiyani pa iwe?”