Salimo 122:1-9

  • Pemphero lopempherera mtendere wa Yerusalemu

    • Anasangalala pamene ankapita kunyumba ya Yehova (1)

    • Mzinda womangidwa ngati chinthu chimodzi chogwirizana (3)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide. 122  Ndinasangalala pamene anandiuza kuti: “Tiyeni tipite kunyumba ya Yehova.”+   Ndipo tsopano mapazi athu aimaPamageti ako iwe Yerusalemu.+   Yerusalemu ndi mzinda umene wamangidwaNgati chinthu chimodzi chogwirizana.+   Mafuko apita kumeneko,Mafuko a Ya,*Mogwirizana ndi chilamulo chimene* Isiraeli anapatsidwaKuti azikatamanda dzina la Yehova.+   Chifukwa kumeneko nʼkumene kunaikidwa mipando yachiweruzo,+Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+   Pemphererani mtendere wa Yerusalemu.+ Amene amakukonda, mzinda iwe, adzakhala otetezeka.   Mtendere upitirize kukhala mʼmalo ako otchingidwa ndi mpanda wolimba,Chitetezo chipitirize kukhala munsanja zako zokhala ndi mpanda wolimba.   Chifukwa choti ndimakonda abale anga komanso anzanga ndikunena kuti: “Mumzindawu mukhale mtendere.”   Chifukwa choti ndimakonda nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+Ndidzapitiriza kukufunira zabwino.

Mawu a M'munsi

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “zikumbutso zimene.”