Salimo 123:1-4

  • Kupempha Yehova kuti awakomere mtima

    • ‘Monga atumiki ake, tikuyangʼana kwa Yehova’ (2)

    • “Tanyozeka kwambiri” (3)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 123  Ndakweza maso anga kuyangʼana inu,+Inu amene mpando wanu wachifumu uli kumwamba.   Mofanana ndi mmene maso a atumiki amayangʼanira dzanja la mbuye wawo,Komanso mmene maso a kapolo wamkazi amayangʼanira dzanja la mbuye wake wamkazi,Maso athu akuyangʼana kwa Yehova Mulungu wathu,+Mpakana atatikomera mtima.+   Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,Chifukwa tanyozeka kwambiri.+   Anthu odzikuza atinyoza kwambiri*Ndipo anthu onyada atichitira zachipongwe.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Zimene anthu odzikuza akutichitira zatikwana.”