Salimo 124:1-8
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.
124 “Yehova akanapanda kukhala nafe,”+
Tsopano Isiraeli anene kuti,
2 “Yehova akanapanda kukhala nafe,+Pamene anthu anatiukira,+
3 Akanatimeza amoyo+Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+
4 Pamenepo madzi akanatikokolola,Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+
5 Madzi amphamvu akanatikokolola.
6 Yehova atamandike,Chifukwa sanatipereke kwa iwo kuti atimbwandire ngati nyama.
7 Tili ngati mbalame imene yathawaPamsampha wa munthu wosaka.+Msamphawo unathyoka,Ndipo ife tinathawa.+
8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova,+Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.”