Salimo 125:1-5

  • Yehova amateteza anthu ake

    • “Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu” (2)

    • “Mu Isiraeli mukhale mtendere” (5)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 125  Anthu amene amakhulupirira Yehova+Ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezekeKoma lidzakhalapo mpaka kalekale.+   Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu,+Yehova wazungulira anthu ake,+Kuyambira panopa mpaka kalekale.   Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala padziko limene laperekedwa kwa anthu olungama,+Kuti olungamawo* asayambe kuchita zinthu zoipa.+   Inu Yehova, anthu abwino muwachitire zabwino,+Muchitire zabwino anthu owongoka mtima.+   Koma anthu amene apatuka panjira yabwino nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zokhotakhota,Yehova adzawachotsa limodzi ndi anthu ochita zoipa.+ Mu Isiraeli mukhale mtendere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “manja a olungamawo.”