Salimo 127:1-5
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Solomo.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+
Yehova akapanda kulondera mzinda,+Alonda amakhala maso pachabe.
2 Mukudzuka mʼmawa pachabe,Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,Mumapeza chakudya movutikira,Chifukwa Mulungu amapereka zinthu zofunika kwa anthu amene amawakonda komanso amawapatsa tulo tabwino.+
3 Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+Chipatso cha mimba ndi mphoto yochokera kwa Mulungu.+
4 Ana a bambo wachinyamata,+Ali ngati mivi mʼdzanja la mwamuna wamphamvu.
5 Wosangalala ndi mwamuna amene wadzaza kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.+
Abambo oterowo sadzachita manyazi,Chifukwa ana awo adzalankhula ndi adani pageti la mzinda.