Salimo 128:1-6

  • Woopa Yehova amasangalala

    • Mkazi wokhala ngati mtengo wa mpesa wobereka zipatso (3)

    • “Uone zinthu zikuyenda bwino mu Yerusalemu” (5)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 128  Wosangalala ndi aliyense amene amaopa Yehova,+Amene amayenda mʼnjira za Mulungu.+   Udzadya zinthu zimene wapeza utagwira ntchito mwakhama. Udzakhala wosangalala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+   Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobereka zipatso mʼnyumba mwako.+Ana ako adzakhala ngati mphukira za mtengo wa maolivi kuzungulira tebulo lako.   Mwamuna aliyense amene amaopa YehovaAdzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+   Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni. Uone zinthu zikuyenda bwino mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+   Ndipo uone ana a ana ako. Mtendere ukhale pa Isiraeli.

Mawu a M'munsi