Salimo 129:1-8

  • Kuukiridwa koma osagonjetsedwa

    • Odana ndi Ziyoni achititsidwa manyazi (5)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 129  “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,”+ Tsopano Isiraeli anene kuti,   “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,+Koma sanandigonjetse.+   Olima ndi ngʼombe andilima pamsana.+Iwo alima mizere italiitali.”   Koma Yehova ndi wolungama.+Iye wadula zingwe za oipa.+   Onse amene amadana ndi Ziyoni,Adzanyozeka ndipo adzabwerera mwamanyazi.+   Adzakhala ngati udzu umene wamera padengaUmene umauma usanazulidwe,   Umene sungadzaze mʼdzanja la munthu amene akukololaKapena mʼmanja mwa munthu amene akumanga mitolo ya zokolola.   Anthu odutsa sadzanena kuti: “Madalitso a Yehova akhale nanu.Tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Mawu a M'munsi