Salimo 13:1-6

  • Kuyembekezera chipulumutso cha Yehova

    • “Mpaka liti, inu Yehova?” (1, 2)

    • Yehova amapereka mphoto yaikulu (6)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 13  Kodi mudzandiiwala mpaka liti, inu Yehova? Mpaka kalekale? Kodi mudzandibisira nkhope yanu mpaka liti?+   Kodi ndidzapitiriza kuvutika ndi nkhawa,Komanso tsiku lililonse ndidzakhala ndi chisoni mumtima mwanga mpaka liti? Kodi mdani wanga adzapambana mpaka liti?+   Ndiyangʼaneni ndipo mundiyankhe, inu Yehova Mulungu wanga. Chititsani maso anga kuti aone kuwala, kuti ndisagone mu imfa.   Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!” Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa chakuti ndagwa.+   Koma ine ndakhulupirira chikondi chanu chokhulupirika+Mtima wanga udzasangalala chifukwa cha chipulumutso chanu.+   Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandipatsa mphoto yaikulu.+

Mawu a M'munsi