Salimo 130:1-8

  • “Pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu”

    • “Mukanakhala kuti mumayangʼanitsitsa zolakwa” (3)

    • Yehova amakhululuka ndi mtima wonse (4)

    • “Ndikuyembekezera Yehova ndi mtima wonse” (6)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 130  Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+   Inu Yehova, imvani mawu anga. Makutu anu amve kuchonderera kwanga kopempha thandizo.   Inu Ya,* mukanakhala kuti mumayangʼanitsitsa* zolakwa,Ndi ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+   Chifukwa inu mumakhululuka ndi mtima wonse,+Kuti anthu azikuopani.+   Ndikuyembekezera Yehova. Moyo wanga wonse ukumuyembekezera.Ine ndikuyembekezera mawu ake.   Ndikuyembekezera Yehova ndi mtima wonse,+Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.   Isiraeli apitirize kuyembekezera Yehova,Chifukwa Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika,+Ndipo ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu.   Iye adzawombola Aisiraeli ku zolakwa zawo zonse.

Mawu a M'munsi

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “mumasunga.”