Salimo 131:1-3

  • Wokhutira ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa

    • “Sindilakalaka zinthu zapamwamba kwambiri” (1)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide. 131  Inu Yehova, mtima wanga si wodzikweza,Maso anga si onyada.+Sindilakalaka zinthu zapamwamba kwambiri,+Kapena zinthu zimene sindingazikwanitse.   Koma ine ndatonthoza mtima wanga ndipo ndaukhazika mʼmalo+Ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa, amene ali mʼmanja mwa mayi ake.Ndine wokhutira ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa.   Isiraeli ayembekezere Yehova,+Kuyambira panopa mpaka kalekale.

Mawu a M'munsi