Salimo 132:1-18

  • Anasankha Davide komanso Ziyoni

    • “Musakane wodzozedwa wanu” (10)

    • Ansembe a ku Ziyoni adzawaveka chipulumutso (16)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 132  Inu Yehova, kumbukirani DavideKomanso mavuto onse amene anakumana nawo.+   Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,Analonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti:+   “Sindidzalowa mutenti yanga, mʼnyumba yanga.+ Sindidzagona pabedi langa.   Sindidzalola kuti ndigoneKapena kutseka maso anga,   Mpaka nditamupezera Yehova malo okhala,Malo abwino oti* Wamphamvu wa Yakobo azikhalamo.”+   Ku Efurata,+ tinamva zimene zinachitika.Tinalipeza kunkhalango.*+   Tiyeni tilowe mʼmalo ake okhala.*+Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+   Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe mʼmalo anu okhalamo,+Inu pamodzi ndi Likasa limene likuimira mphamvu zanu.+   Ansembe anu avale chilungamo,Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala. 10  Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,Musakane* wodzozedwa wanu.+ 11  Yehova walumbira kwa Davide.Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti: “Ndidzaika pampando wako wachifumuMmodzi wa ana ako.*+ 12  Ana ako akadzasunga pangano langaKomanso malamulo* anga amene ndikuwaphunzitsa,+Ana awonsoAdzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+ 13  Chifukwa Yehova wasankha Ziyoni.+Akufunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye akuti:+ 14  “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka kalekale.Ndidzakhala mmenemu,+ chifukwa zimenezi ndi zimene ndikulakalaka. 15  Ndidzadalitsa kwambiri malo amenewa ndi chakudya.Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+ 16  Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+Ndipo okhulupirika ake adzafuula mosangalala.+ 17  Kumeneko ndidzachulukitsa mphamvu* za Davide. Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+ 18  Adani ake ndidzawaveka manyazi,Koma ufumu wake udzakhala wamphamvu.”*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Chihema chachikulu choti.”
Nʼkutheka kuti akunena zokhudza Likasa.
Kapena kuti, “tilowe mʼchihema chake chachikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Musabweze nkhope ya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yako.”
Kapena kuti, “zikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chake chachifumu chidzakhala champhamvu.”