Salimo 133:1-3

  • Kukhala pamodzi mogwirizana

    • Ngati mafuta pamutu wa Aroni (2)

    • Ngati mame a ku Herimoni (3)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide. 133  Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiriAbale akakhala pamodzi mogwirizana!+   Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu+Amene akuyenderera pandevu,Ndevu za Aroni,+Ndipo akuyenderera mpaka mʼkolala ya zovala zake.   Zili ngati mame a ku Herimoni,+Amene akutsikira pamapiri a ku Ziyoni.+ Kumeneko nʼkumene Yehova analonjeza kuti kudzakhala madalitso ake,Omwe ndi moyo wosatha.

Mawu a M'munsi