Salimo 135:1-21

  • Tamandani Ya chifukwa ndi wamkulu

    • Zizindikiro komanso zodabwitsa ku Iguputo (8, 9)

    • “Dzina lanu lidzakhalapo kwamuyaya” (13)

    • Mafano opanda moyo (15-18)

135  Tamandani Ya!* Tamandani dzina la Yehova,Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+   Inu amene mwaimirira mʼnyumba ya Yehova,Mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+   Tamandani Ya, chifukwa Yehova ndi wabwino.+ Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, chifukwa kuchita zimenezi nʼkosangalatsa.   Ya wasankha Yakobo kuti akhale wake,Wasankha Isiraeli kuti akhale chuma chake chapadera.*+   Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu.Ambuye wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.+   Yehova amachita chilichonse chimene wafuna+Kumwamba, padziko lapansi, mʼnyanja komanso mʼmalo onse ozama.   Amachititsa kuti mitambo* ikwere kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima.Amatulutsa mphepo kuchokera mʼnyumba zake zosungira zinthu.+   Iye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,Ana a anthu komanso ana a nyama.+   Anachita zizindikiro komanso zodabwitsa pakati pako, iwe Iguputo,+Anachita zimenezi kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+ 10  Anawononga mitundu yambiri+Ndipo anapha mafumu amphamvu+ 11  Anapha Sihoni mfumu ya Aamori,+Ogi mfumu ya Basana+Komanso anawononga maufumu onse a ku Kanani. 12  Dziko lawo analipereka kuti likhale cholowa,Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+ 13  Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo kwamuyaya. Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo* ku mibadwo yonse.+ 14  Chifukwa Yehova adzateteza anthu ake pa mlandu,*+Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+ 15  Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,Ntchito ya manja a anthu.+ 16  Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+Maso ali nawo koma sangaone. 17  Makutu ali nawo koma sangamve. Mʼkamwa mwawo mulibe mpweya.+ 18  Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+ 19  Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova. Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova. 20  Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+ Inu amene mumaopa Yehova, tamandani Yehova. 21  Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+Atamandidwe mu Ziyoni.+ Tamandani Ya!+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “chamtengo wapatali.”
Kapena kuti, “nthunzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chanu chidzakhalapo.”
Kapena kuti, “adzaweruzira anthu ake mlandu.”