Salimo 136:1-26

  • Chikondi chokhulupirika cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale

    • Kumwamba ndi dziko lapansi zinapangidwa modabwitsa (5, 6)

    • Farao anafera pa Nyanja Yofiira (15)

    • Mulungu amakumbukira anthu amene afooka (23)

    • Chakudya cha chamoyo chilichonse (25)

136  Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+   Yamikani Mulungu wa milungu,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Yamikani Mbuye wa ambuye,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Iye yekha ndi amene amachita ntchito zazikulu zodabwitsa,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+   Iye anapanga kumwamba mwaluso,*+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Iye anapanga zounikira zazikulu,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.   Anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 10  Iye anapha ana oyamba kubadwa a Aiguputo,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 11  Iye anatulutsa Aisiraeli pakati pawo,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale, 12  Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu+ komanso mkono wotambasula,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 13  Iye anagawa pakati Nyanja Yofiira,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 14  Anachititsa kuti Isiraeli adutse pakati pake,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 15  Anakutumulira Farao ndi asilikali ake mʼNyanja Yofiira,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 16  Iye anatsogolera anthu ake mʼchipululu,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 17  Anapha mafumu akuluakulu,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 18  Anapha mafumu amphamvu,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale, 19  Sihoni+ mfumu ya Aamori,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale, 20  Komanso Ogi+ mfumu ya Basana,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 21  Iye anapereka dziko lawo kwa anthu ake kuti likhale cholowa,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale, 22  Kuti likhale cholowa cha Isiraeli mtumiki wake,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 23  Iye anatikumbukira pa nthawi imene tinali ofooka,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+ 24  Anapitiriza kutipulumutsa kwa adani athu,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 25  Amapereka chakudya kwa zamoyo zonse,+Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. 26  Yamikani Mulungu wakumwamba,Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mwanzeru.”