Salimo 137:1-9

  • Mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo

    • Palibe nyimbo za ku Ziyoni zimene zinaimbidwa (3, 4)

    • Babulo adzawonongedwa (8)

137  Tinakhala pansi mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo.+ Tinalira titakumbukira Ziyoni.+   Tinapachika azeze athu+Pamitengo ya msondodzi imene inali mmenemo.*   Chifukwa kumeneko, anthu amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+Amene ankatinyozawo ankafuna kuti tiwasangalatse. Iwo anati: “Tiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.”   Tingaimbe bwanji nyimbo ya YehovaMʼdziko lachilendo?   Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.+   Lilime langa limamatire mʼkamwa mwangaNgati sindingakukumbukire,Ngati sindingaike Yerusalemu pamwambaPa chilichonse chimene chimandisangalatsa kwambiri.+   Inu Yehova, kumbukiraniZimene Aedomu ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa. Iwo anati: “Gwetsani mzindawo! Ugwetseni mpaka pamaziko ake!”+   Iwe mwana wamkazi wa Babulo,* amene watsala pangʼono kuwonongedwa,+Wosangalala adzakhala amene adzakubwezereZimene iwe watichitira.+   Wosangalala adzakhala amene adzagwire ana akoNʼkuwaphwanya powawombetsa pathanthwe.+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza mu Babulo.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.