Salimo 14:1-7

  • Zimene opusa amachita

    • “Kulibe Yehova” (1)

    • “Palibe aliyense amene akuchita zabwino” (3)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 14  Munthu wopusa* amanena mumtima mwake kuti: “Kulibe Yehova.”+ Zochita za anthu amenewa ndi zoipa komanso zonyansa,Ndipo palibe amene akuchita zabwino.+   Koma kuchokera kumwamba, Yehova amayangʼana ana a anthu,Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, ngati pali aliyense amene akufunafuna Yehova.+   Onse apatuka,+Ndipo onsewo ndi achinyengo. Palibe aliyense amene akuchita zabwino,Palibiretu ndi mmodzi yemwe.   Kodi palibe aliyense womvetsa zinthu pakati pa anthu ochita zoipawa? Iwo amadya anthu anga ngati kuti akudya chakudya. Ndipo sapemphera kwa Yehova.   Koma adzagwidwa ndi mantha aakulu,+Chifukwa Yehova ali pakati pa mʼbadwo wa anthu olungama.   Inu anthu ochita zoipa mumayesetsa kusokoneza mapulani a munthu wonyozeka,Koma Yehova ndi malo ake othawirako.+   Zikanakhala bwino chipulumutso cha Isiraeli chikanachokera ku Ziyoni.+ Yehova akadzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wopanda nzeru.”