Salimo 140:1-13

  • Yehova ndi Mpulumutsi wamphamvu

    • Anthu oipa ali ngati njoka (3)

    • Anthu ankhanza adzagwa (11)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 140  Inu Yehova, ndipulumutseni kwa anthu oipa.Nditetezeni kwa anthu ochita zachiwawa,+   Anthu amene amakonza chiwembu mʼmitima yawo+Ndipo amayambitsa mikangano tsiku lonse.   Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+Mʼmilomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ (Selah)   Inu Yehova, nditetezeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+Nditetezeni kwa anthu amene amachita zachiwawa.Amene amakonza chiwembu kuti andivulaze.   Anthu onyada anditchera msampha.Iwo agwiritsa ntchito zingwe kuti atchere ukonde mʼmphepete mwa njira,+ Ndipo anditchera makhwekhwe.+ (Selah)   Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga. Mvetserani inu Yehova, kuchonderera kwanga kopempha thandizo.”+   Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, Mpulumutsi wanga wamphamvu,Mwateteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+   Inu Yehova, musapatse anthu oipa zimene amalakalaka. Musalole kuti ziwembu zawo zitheke kuti angayambe kunyada.+ (Selah)   Mitu ya anthu amene andizunguliraIphimbidwe ndi zoipa zimene amalankhula.+ 10  Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+ Aponyedwe pamoto,Mʼmaenje akuya*+ ndipo asadzukenso. 11  Munthu wonenera anzake zoipa asapeze malo padziko lapansi.*+ Zoipa zisakesake anthu ochita zachiwawa ndipo ziwawononge. 12  Ndikudziwa kuti Yehova adzateteza anthu onyozeka pa mlandu wawoNdipo adzachitira chilungamo anthu osauka.+ 13  Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.Anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mʼmaenje a madzi.”
Kapena kuti, “mʼdziko.”