Salimo 141:1-10

  • Pemphero lopempha kuti atetezedwe

    • “Pemphero langa likhale ngati zofukiza” (2)

    • Kudzudzulidwa ndi munthu wolungama kuli ngati mafuta (5)

    • Oipa adzagwera mʼmaukonde awo omwe (10)

Nyimbo ya Davide. 141  Inu Yehova, ine ndakuitanani.+ Bwerani mofulumira kuti mudzandithandize.+ Mutchere khutu ndikamakuitanani.+   Pemphero langa likhale ngati zofukiza+ zokonzedwa pamaso panu,+Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+   Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.Ikani woti azilondera patsogolo pa milomo yanga.+   Musalole kuti mtima wanga uzikonda chinthu chilichonse choipa,+Komanso kuti ndizichita zinthu zoipa limodzi ndi anthu oipa.Sindikufuna kudya chakudya chawo chapamwamba.   Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza chikondi chokhulupirika.+Akandidzudzula zingakhale ngati wandidzoza mafuta pamutu,+Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+ Ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.   Ngakhale oweruza awo atawagwetsera pansi kuchokera pathanthwe,Anthu adzamvetsera mawu anga chifukwa ndi osangalatsa.   Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,*Mofanana ndi dothi limene limamwazika munthu akamalima.   Koma ine maso anga ali pa inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ Ine ndathawira kwa inu. Musachotse moyo wanga.   Nditetezeni kuti ndisagwidwe pamsampha umene anditchera,Kuti ndisakodwe ndi makhwekhwe a anthu ochita zoipa. 10  Oipa onse adzagwera mʼmaukonde awo omwe,+Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

Mawu a M'munsi

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.