Salimo 144:1-15

  • Pemphero lopempha kupulumutsidwa

    • ‘Munthu ndi ndani?’ (3)

    • ‘Adani achite mantha’ (6)

    • Osangalala ndi anthu a Yehova (15)

Salimo la Davide. 144  Atamandike Yehova Thanthwe langa,+Amene amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,Komanso zala zanga kumenyana ndi adani anga.+   Iye amandisonyeza chikondi chake chokhulupirika ndipo ndi malo anga otetezeka,Malo anga othawirako otetezeka* komanso amene amandipulumutsa,Chishango changa ndiponso malo amene ndathawirako kuti nditetezeke,+Amene amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera.+   Inu Yehova, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira?Kodi mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimuwerengera?+   Munthu amafanana ndi mpweya.+Masiku a moyo wake ali ngati mthunzi wongodutsa.+   Inu Yehova, tsitsani* kumwamba ndipo mutsike.+Khudzani mapiri ndipo muwachititse kuti afuke utsi.+   Chititsani kuti mphezi zingʼanime kuti adani abalalike.+Ponyani mivi yanu ndipo muwasokoneze.+   Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.Ndilanditseni ndi kundipulumutsa mʼmadzi amphamvu,Ndilanditseni mʼmanja mwa anthu achilendo,+   Amene amalankhula zinthu zabodzaKomanso amene amakweza dzanja lawo lamanja kuti alumbire mwachinyengo.*   Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+ Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10. 10  Ndidzaimbira inu amene mumathandiza mafumu kuti apambane,*+Inu amene mumapulumutsa Davide mtumiki wanu kuti asaphedwe ndi lupanga.+ 11  Ndilanditseni ndi kundipulumutsa mʼmanja mwa anthu achilendo,Amene amalankhula zinthu zabodzaKomanso amakweza dzanja lawo lamanja kuti alumbire mwachinyengo. 12  Mukatero ana athu aamuna adzakhala ngati mitengo ingʼonoingʼono imene ikukula mofulumira,Ndipo ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zamʼmakona zosemedwa mwaluso, kuti akazigwiritse ntchito pomanga nyumba yachifumu. 13  Nyumba zathu zosungiramo zinthu zizadzaza ndi zokolola zamitundu yosiyanasiyana.Nkhosa zathu zidzaswana nʼkukhala masauzandemasauzande kapena masauzande ambirimbiri. 14  Ngʼombe zathu zimene zili ndi bere, sizidzavulala kapena kubereka ana akufa.Ndipo mʼmabwalo athu simudzamveka kulira kwa munthu amene ali pamavuto. 15  Osangalala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira. Osangalala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Malo okwezeka achitetezo.”
Kapena kuti, “weramitsani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo dzanja lawo lamanja ndi dzanja lamanja lachinyengo.”
Kapena kuti, “apulumuke.”