Salimo 147:1-20

  • Kutamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zachikondi komanso zamphamvu

    • Amachiritsa anthu osweka mtima (3)

    • Amatchula dzina nyenyezi iliyonse (4)

    • Amapereka sinowo ngati ubweya wa nkhosa (16)

147  Tamandani Ya!* Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda nʼkwabwino,Kumutamanda nʼkosangalatsa komanso koyenera.+   Yehova akumanga Yerusalemu.+Akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli amene anapita ku ukapolo.+   Iye amachiritsa anthu osweka mtima,Ndipo amamanga mabala awo.   Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse,Ndipo iliyonse amaitchula dzina lake.+   Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.+Nzeru zake zilibe malire.+   Yehova amakweza anthu ofatsa,+Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.   Imbirani Yehova nyimbo moyamikira.Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze.   Imbirani amene amaphimba mapiri ndi mitambo,Amene amapereka mvula padziko lapansi,+Amenenso amameretsa udzu+ mʼmapiri.   Iye amapereka chakudya kwa zinyama,+Amapatsa ana a makwangwala chakudya chimene akulirira.+ 10  Iye sachita chidwi ndi mphamvu za hatchi,+Kapena miyendo ya munthu yomwe ndi yamphamvu.+ 11  Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.+ 12  Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. 13  Amachititsa kuti mipiringidzo ya mageti ako ikhale yolimba.Ndipo amadalitsa ana ako. 14  Iye amabweretsa mtendere mʼdziko lako.+Ndipo amakupatsa tirigu wabwino* kwambiri.+ 15  Amapereka lamulo lake padziko lapansi.Mawu ake amathamanga mofulumira kwambiri. 16  Iye amapereka sinowo* ngati ubweya wa nkhosa.+Amamwaza mame oundana ngati phulusa.+ 17  Amaponya matalala ake ngati nyenyeswa za chakudya.+ Ndi ndani angapirire kuzizira kwake?+ 18  Amatumiza mawu ake ndipo matalalawo amasungunuka. Amachititsa mphepo yake kuwomba,+ ndipo madzi amayenda. 19  Yakobo amamuuza mawu ake,Ndipo Isiraeli amamuuza malangizo ake komanso zigamulo zake.+ 20  Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake. Tamandani Ya!*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amakupatsa mafuta a tirigu.”
Kapena kuti, “chipale chofewa.”
Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.