Salimo 24:1-10
-
Mfumu yaulemerero yalowa mʼmageti
-
‘Dziko lapansi ndi la Yehova’ (1)
-
Salimo la Davide. Nyimbo.
24 Dziko lapansi ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova,+Nthaka komanso onse okhala panthakapo ndi ake.
2 Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja+Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.
3 Ndi ndani angakwere kuphiri la Yehova,+Ndipo ndi ndani angaime mʼmalo ake opatulika?
4 Aliyense amene ndi wosalakwa komanso wopanda chinyengo mumtima mwake,+Amene sanalumbire mwachinyengo potchula moyo Wanga,*Kapena kulumbira pofuna kupusitsa anthu ena.+
5 Iye adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+Komanso chilungamo kuchokera kwa Mulungu amene amamupulumutsa.+
6 Umenewu ndi mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna Mulungu,Mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo. (Selah)
7 Tukulani mitu yanu, inu mageti,+Tsegukani,* inu makomo akale,Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!+
8 Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani?
Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+Yehova, wamphamvu pankhondo.+
9 Tukulani mitu yanu, inu mageti,+Tsegukani, inu makomo akale,Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!
10 Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani?
Ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Iye ndi Mfumu yaulemerero.+ (Selah)