Salimo 25:1-22

  • Pemphero lopempha kutsogoleredwa komanso kukhululukidwa

    • “Ndiphunzitseni njira zanu” (4)

    • “Ubwenzi wolimba ndi Yehova” (14)

    • “Mundikhululukire machimo anga onse” (18)

Salimo la Davide. א [Aleph] 25  Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova. ב [Beth]  2  Inu Mulungu wanga, ndimakudalirani.+Musalole kuti ndichite manyazi.+ Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.+ ג [Gimel]  3  Ndithudi, palibe anthu amene amayembekezera inu amene adzachite manyazi.+Koma amene adzachite manyazi ndi anthu amene amachita zachinyengo popanda chifukwa.+ ד [Daleth]  4  Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+Ndiphunzitseni kuyenda mʼnjira zanu.+ ה [He]  5  Ndithandizeni kuti ndiziyenda mʼchoonadi chanu ndipo mundiphunzitse,+Chifukwa inu ndinu Mulungu amene mumandipulumutsa. ו [Waw] Ndimayembekezera inu tsiku lonse. ז [Zayin]  6  Kumbukirani chifundo chanu, inu Yehova, komanso chikondi chanu chokhulupirika,+Zimene mumasonyeza nthawi zonse.*+ ח [Heth]  7  Musakumbukire machimo amene ndinachita ndili mnyamata komanso zolakwa zanga. Mundikumbukire chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova,+Mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+ ט [Teth]  8  Yehova ndi wabwino komanso wolungama.+ Nʼchifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende mʼnjira yoyenera.+ י [Yod]  9  Adzatsogolera ofatsa kuti azichita zinthu zoyenera,+Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuti aziyenda mʼnjira yake.+ כ [Kaph] 10  Njira zonse za Yehova ndi zokhulupirika ndipo nʼzogwirizana ndi chikondi chake chokhulupirikaKwa anthu amene amasunga pangano lake+ ndi zikumbutso zake.+ ל [Lamed] 11  Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+Mundikhululukire tchimo langa, ngakhale kuti ndi lalikulu. מ [Mem] 12  Ngati munthu amaopa Yehova,+ Iye adzamulangiza njira imene akuyenera kusankha.+ נ [Nun] 13  Moyo wake udzasangalala ndi zinthu zabwino,+Ndipo mbadwa* zake zidzatenga dziko lapansi kuti likhale lawo.+ ס [Samekh] 14  Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba,+Ndipo amawadziwitsa pangano lake.+ ע [Ayin] 15  Maso anga amayangʼana kwa Yehova nthawi zonse,+Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+ פ [Pe] 16  Tembenukani nʼkundiyangʼana ndipo mundikomere mtima.Chifukwa ndili ndekhandekha ndipo ndilibe wondithandiza. צ [Tsade] 17  Nkhawa zamumtima mwanga zawonjezeka.+Ndipulumutseni ku mavuto anga. ר [Resh] 18  Onani mavuto ndi masautso anga,+Ndipo mundikhululukire machimo anga onse.+ 19  Onani mmene adani anga achulukira,Komanso onani kuti amadana nane kwambiri. ש [Shin] 20  Tetezani moyo wanga ndipo mundipulumutse.+ Musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndathawira kwa inu. ת [Taw] 21  Kukhala wokhulupirika komanso kuchita zinthu zoyenera kunditeteze,+Chifukwa chiyembekezo changa chili mwa inu.+ 22  Inu Mulungu, pulumutsani* Isiraeli ku mavuto ake onse.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Zimene munayamba kuchita kale kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wombolani.”