Salimo 26:1-12
Salimo la Davide.
26 Ndiweruzeni, inu Yehova, chifukwa ndimachita zinthu mokhulupirika.+Nthawi zonse ndimadalira inu Yehova.+
2 Ndifufuzeni, inu Yehova, ndipo mundiyese.Yengani maganizo anga* komanso mtima wanga.+
3 Chifukwa nthawi zonse ndimaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,Ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu.+
4 Sindicheza* ndi anthu achinyengo,+Ndipo ndimapewa anthu amene amabisa umunthu wawo.*
5 Ndimadana ndi zokhala pagulu la anthu ochita zoipa,+Ndipo ndimakana kucheza* ndi anthu oipa.+
6 Ndidzasamba mʼmanja mwanga kusonyeza kuti ndine wosalakwa,Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,
7 Kuti mawu anga oyamikira amveke,+Komanso kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zodabwitsa.
8 Yehova, ndimakonda nyumba imene inu mumakhala,+Malo amene kumakhala ulemerero wanu.+
9 Musandiwononge limodzi ndi anthu ochimwa,+Kapena kuchotsa moyo wanga limodzi ndi anthu achiwawa.*
10 Amene manja awo amachita khalidwe lochititsa manyazi,Ndipo mʼdzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.
11 Koma ine, ndidzapitiriza kuchita zinthu mokhulupirika.
Ndipulumutseni* ndipo mundikomere mtima.
12 Phazi langa laima pamalo otetezeka.+Ndidzatamanda Yehova mumpingo* waukulu.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindikhala pansi.”
^ Kapena kuti, “Sindichita zinthu limodzi ndi anthu achinyengo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala pansi.”
^ Kapena kuti, “anthu a mlandu wa magazi.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “pamsonkhano.”