Salimo 27:1-14

  • Yehova amateteza moyo wanga

    • Kuyamikira kachisi wa Mulungu (4)

    • Yehova amatisamalira ngakhale makolo athu atatisiya (10)

    • “Yembekezera Yehova” (14)

Salimo la Davide. 27  Yehova ndi kuwala kwanga+ komanso ndi amene amandipulumutsa. Ndingaope ndani?+ Yehova ali ngati malo amene amateteza moyo wanga.+ Ndingachite mantha ndi ndani?   Anthu oipa atandiukira kuti adye mnofu wanga,+Adani angawo ndi amene anapunthwa nʼkugwa.   Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,Mtima wanga sudzachita mantha.+ Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,Pameneponso ndidzadalira Mulungu.   Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+   Chifukwa pa tsiku la tsoka, adzandibisa mʼmalo ake otetezeka.+Adzandibisa mʼmalo obisika a mutenti yake.+Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+   Tsopano ndapambana pamaso pa adani anga onse amene andizungulira.Ndidzapereka nsembe patenti yake ndikufuula mosangalala.Ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.   Inu Yehova, ndimvetsereni pamene ndikuitana.+Ndikomereni mtima ndipo mundiyankhe.+   Mtima wanga wandikumbutsa za lamulo lanu lakuti: “Funafunani nkhope yanga anthu inu.” Ndidzafunafuna nkhope yanu, inu Yehova.+   Musandibisire nkhope yanu.+ Musabweze mtumiki wanu mutakwiya. Inu ndi amene mumandithandiza.+Musanditaye kapena kundisiya, inu Mulungu amene mumandipulumutsa. 10  Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+Yehova adzanditenga.+ 11  Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende mʼnjira yanu.+Nditsogolereni mʼnjira yoyenera kuti nditetezeke kwa adani anga. 12  Musandipereke kwa adani anga,+Chifukwa mboni zabodza zikundinamizira mlandu,+Ndipo akundiopseza kuti andichitira zachiwawa. 13  Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriroChoti ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo?*+ 14  Yembekezera Yehova.+Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+ Inde, yembekezera Yehova.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo opatulika ake.”
Kapena kuti, “Komanso kuti ndiyangʼane ndi kuganizira mozama za kachisi wake.”
Mabaibulo ena amati, “Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.”