Salimo 28:1-9

  • Mulungu anayankha pemphero la amene analemba salimo

    • ‘Yehova ndi mphamvu yanga komanso chishango changa’ (7)

Salimo la Davide. 28  Ndikuitana inu Yehova, Thanthwe langa,+Musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana. Mukakhala chete pamene ndikukuitanani,Ndidzafanana ndi anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+   Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,Pamene ndikukweza manja anga, nditayangʼana kumene kuli chipinda chamkati chamʼmalo anu opatulika.+   Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa, amene amachita zopweteka anzawo,+Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo, koma mʼmitima yawo muli zinthu zoipa.+   Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+Mogwirizana ndi zochita zawo zoipa. Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo,Mogwirizana ndi zimene achita.+   Chifukwa iwo sachita chidwi ndi zochita za Yehova,+Kapena ntchito za manja ake.+ Mulungu adzawagwetsa ndipo sadzawamanga.   Atamandike Yehova,Chifukwa iye wamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo.   Yehova ndi mphamvu yanga+ komanso chishango changa.+Mtima wanga umamukhulupirira.+ Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukusangalala.Choncho ndidzamutamanda ndi nyimbo yanga.   Yehova ndi mphamvu kwa anthu ake,Iye ndi malo achitetezo, amapereka chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+   Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+ Mukhale mʼbusa wawo ndipo muwanyamule mʼmanja mwanu mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi