Salimo 29:1-11

  • Mawu a Yehova ndi amphamvu

    • Lambirani Mulungu mutavala zovala zopatulika zokongola (2)

    • “Mulungu waulemerero akugunda ngati bingu” (3)

    • Yehova amapatsa anthu ake mphamvu (11)

Nyimbo ya Davide. 29  Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu ana a amphamvu,Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+   Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Weramirani* Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.*   Mawu a Yehova akumveka pamwamba pa madzi,Mawu a Mulungu waulemerero akugunda ngati bingu.+ Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+   Mawu a Yehova ndi amphamvu,+Mawu a Yehova ndi aulemerero.   Mawu a Yehova akuthyola mitengo ya mkungudza,Inde, Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+   Iye akuchititsa Lebanoni* kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe,Komanso Sirioni+ kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe yakutchire.   Yehova akamalankhula, mphenzi zimangʼanima.+   Mawu a Yehova akuchititsa kuti chipululu chiphiriphithe,+Yehova akuchititsa kuti chipululu cha Kadesi+ chiphiriphithe.   Mawu a Yehova akuchititsa kuti mbawala zazikazi ziphiriphithe kenako nʼkuberekaNdipo akuchititsa kuti munkhalango mukhale mopanda chilichonse.+ Ndipo onse mʼkachisi wake akunena kuti: “Ulemerero!” 10  Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa madzi osefukira,*+Yehova ndi Mfumu ndipo adzalamulira mpaka kalekale.+ 11  Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+ Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendere.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Lambirani.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha kukongola kwa chiyero chake.”
Zikuoneka kuti akunena za phiri la Lebanoni.
Kapena kuti, “pa nyanja yaikulu yakumwamba.”