Salimo 30:1-12
-
Kulira kunasanduka chisangalalo
-
Mulungu amakomera mtima anthu kwa moyo wawo wonse (5)
-
Nyimbo yotsegulira nyumba. Salimo la Davide.
30 Ndidzakutamandani inu Yehova, chifukwa mwandipulumutsa.*Simunalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.+
2 Inu Yehova Mulungu wanga, ndinafuulira kwa inu kuti mundithandize ndipo munandichiritsa.+
3 Inu Yehova, mwanditulutsa mʼManda,*+
Mwandisunga ndi moyo, mwanditeteza kuti ndisatsikire mʼdzenje.*+
4 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, inu okhulupirika ake,+Yamikani dzina* lake loyera.+
5 Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+Koma munthu amene wasangalala naye* amamukomera mtima kwa moyo wake wonse.+
Munthu akhoza kulira usiku, koma mʼmawa amafuula mosangalala.+
6 Pa nthawi imene ndinalibe mavuto ndinanena kuti:
“Sindidzagwedezeka.”*
7 Inu Yehova, pa nthawi imene munkasangalala nane,* munachititsa kuti ndikhale wamphamvu ngati phiri.+
Koma mutabisa nkhope yanu, ndinachita mantha.+
8 Ndinapitiriza kuitana inu Yehova,+Ndipo ndinapitiriza kuchonderera Yehova kuti andikomere mtima.
9 Kodi imfa yanga ili* ndi phindu lanji? Kodi pali phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda?+
Kodi fumbi lingakutamandeni?+ Kodi lingalengeze kuti inu ndinu wokhulupirika?+
10 Imvani inu Yehova, ndipo mundikomere mtima.+
Inu Yehova, ndithandizeni.+
11 Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.Mwandivula chiguduli changa ndipo mwandiveka chisangalalo,
12 Kuti ndiimbe nyimbo zokutamandani ndipo ndisakhale chete.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani mpaka kalekale.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “mwanditulutsa mʼdzenje.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “mʼmanda.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso.”
^ Kapena kuti, “amene akumufunira zabwino.”
^ Kapena kuti, “Sindidzadzandira.”
^ Kapena kuti, “munkandifunira zabwino.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “magazi anga ali.”