Salimo 35:1-28

  • Pemphero lopempha kupulumutsidwa kwa adani

    • Adani athamangitsidwe (5)

    • Kutamanda Mulungu pakati pa anthu ambiri (18)

    • Kudedwa popanda chifukwa (19)

Salimo la Davide. 35  Inu Yehova, nditetezeni kwa anthu amene akundiimba mlandu.+Menyanani ndi anthu amene akumenyana ndi ine.+   Tengani chishango chanu chachingʼono ndi chachikulu,+Ndipo nyamukani ndi kunditeteza.+   Tengani mkondo ndi nkhwangwa yapankhondo kuti mulimbane ndi adani anga amene akundithamangitsa.+ Ndiuzeni kuti:* “Ine ndine chipulumutso chako.”+   Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi komanso anyozeke.+ Amene akukonza chiwembu choti andiphe abwerere mwamanyazi.   Akhale ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo,Mngelo wa Yehova awathamangitse.+   Njira yawo ikhale yamdima ndi yotereraPamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.   Popanda chifukwa, iwo atchera ukonde kuti andikole.Akumba dzenje kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.   Tsoka liwagwere modzidzimutsa,Akodwe mu ukonde umene atchera okha.Agweremo nʼkufa.+   Koma ine ndidzakondwera chifukwa cha zimene Yehova wachita.Ndidzasangalala chifukwa wandipulumutsa. 10  Ndinena ndi mtima wanga wonse kuti: “Inu Yehova, ndi ndani angafanane ndi inu? Mumapulumutsa anthu ovutika mʼmanja mwa anthu amphamvu kuposa iwowo.+Mumapulumutsa anthu ovutika komanso anthu osauka kwa anthu amene akuwalanda zinthu zawo.”+ 11  Mboni zoipa mtima zabwera,+Ndipo zikundifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa. 12  Iwo amandibwezera zoipa mʼmalo mwa zabwino,+Ndipo ndimakhala wachisoni ngati namfedwa. 13  Koma akadwala ndinkavala chiguduli,Ndinkasala kudya posonyeza kudzichepetsa.Ndipo pemphero langa likapanda kuyankhidwa, 14  Ndinkayendayenda ndikulira ngati kuti ndikulira maliro a mnzanga kapena mchimwene wanga,Ndinkawerama chifukwa cha chisoni ngati munthu amene akulira maliro a mayi ake. 15  Koma nditapunthwa anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.Anasonkhana pamodzi kuti andibisalire nʼkundiukira.Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete. 16  Anthu osaopa Mulungu akundinyoza mwachipongwe,Iwo akundikukutira mano.+ 17  Inu Yehova, kodi mudzayangʼanira zimenezi mpaka liti?+ Ndipulumutseni kuti asandiphe,+Pulumutsani moyo wanga,* womwe ndi wamtengo wapatali, kwa mikango yamphamvu.*+ 18  Mukatero, ndidzakuyamikirani mumpingo waukulu.+Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri. 19  Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa+ asangalale chifukwa cha mavuto anga.Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa andipsinyire diso mondinyoza.+ 20  Chifukwa iwo salankhula mwamtendere,Koma mwachinyengo, amakonzera chiwembu anthu okonda mtendere amʼdzikoli.+ 21  Iwo amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane,Iwo amati: “Eya! Eya! Taona tokha ndi maso athuwa.” 22  Inu Yehova, mwaona zimenezi. Choncho musakhale chete.+ Inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+ 23  Khalani tcheru ndipo nyamukani ndi kunditeteza,Inu Mulungu wanga Yehova, nditetezeni pa mlandu wanga. 24  Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi mfundo zanu zolungama,+Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga. 25  Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Tapeza zimene timafuna.” Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+ 26  Onsewo achite manyazi nʼkuthedwa nzeru,Onse amene amasangalala tsoka likandigwera. Onse amene amadzikweza pamaso panga atsitsidwe ndipo achite manyazi. 27  Koma amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala.Nthawi zonse azinena kuti: “Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pamtendere.”+ 28  Ndipo lilime langa lidzafotokoza* za chilungamo chanu,+Komanso kukutamandani tsiku lonse.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Uzani moyo wanga kuti.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wanga wokhawu,” kutanthauza moyo wake.
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “lidzaganizira mozama.”