Salimo 36:1-12

  • Chikondi chokhulupirika cha Mulungu ndi chamtengo wapatali

    • Woipa saopa Mulungu (1)

    • Mulungu ndi kasupe wa moyo (9)

    • “Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, timaona kuwala” (9)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. 36  Uchimo umalankhula mumtima mwa munthu woipa, nʼkumuuza zochita.Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+   Iye amadziona kuti ndi wofunika kwambiri,Moti sazindikira zolakwa zake nʼkudana nazo.+   Mawu apakamwa pake ndi opweteka komanso achinyengo.Iye amasonyeza kuti alibe nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.   Ngakhale ali pabedi lake, amakonza chiwembu kuti apweteke anzake. Amayenda panjira yoipa,Ndipo sapewa kuchita zinthu zoipa.   Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chafika kumwamba.+Kukhulupirika kwanu kwafika mpaka mʼmitambo.   Chilungamo chanu chili ngati mapiri akuluakulu.*+Ziweruzo zanu zili ngati madzi ambiri ozama.+ Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+   Inu Mulungu, chikondi chanu chokhulupirika ndi chamtengo wapatali!+ Ana a anthu amabisala mumthunzi wa mapiko anu.+   Amamwa zakumwa zabwino* zamʼnyumba yanu nʼkukhuta.+Ndipo mumawachititsa kuti amwe zinthu zanu zosangalatsa zimene zimayenda ngati mtsinje.+   Inu ndinu kasupe wa moyo.+Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, timaona kuwala.+ 10  Pitirizani kusonyeza chikondi chanu chokhulupirika kwa anthu amene amakudziwani,+Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+ 11  Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindiponderezeKapena kuti dzanja la anthu oipa lindithamangitse. 12  Onani, anthu ochita zoipa agwa.Awagwetsera pansi ndipo sangathenso kudzuka.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “chili ngati mapiri a Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zamafuta.”