Salimo 39:1-13

  • Moyo ndi waufupi

    • Munthu ali ngati mpweya (5, 11)

    • “Musanyalanyaze misozi yanga” (12)

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide. 39  Ine ndinanena kuti: “Ndidzakhala wosamala ndi zochita zangaKuti ndisachimwe ndi lilime langa.+ Ndidzaphimba pakamwa panga kuti ndisalankhule+Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”   Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+Sindinalankhule kanthu ngakhale kokhudza zinthu zabwino,Koma ululu wanga unali waukulu.   Mumtima mwanga munayaka moto.* Ndili mkati moganizira,* moto unapitiriza kuyaka. Kenako ndinanena kuti:   “Inu Yehova, ndithandizeni kuzindikira kuti moyo wanga ndi waufupi,Komanso kudziwa chiwerengero cha masiku anga,+Kuti ndidziwe kuti moyo wanga ndi waufupi bwanji.*   Ndithudi, mwachepetsa masiku a moyo wanga,+Ndipo masiku a moyo wanga si kanthu pamaso panu.+ Ndithudi, munthu aliyense ngakhale ataoneka kuti ndi wotetezeka, amangokhala ngati mpweya.+ (Selah)   Zoonadi, moyo wa munthu aliyense umangodutsa ngati chithunzithunzi. Iye amangovutika* popanda phindu. Amaunjika chuma, osadziwa kuti amene adzasangalale nacho ndi ndani.+   Ndiyeno inu Yehova, kodi ine ndikuyembekezera chiyani? Chiyembekezo changa ndi inu nokha.   Ndipulumutseni ku zolakwa zanga zonse.+ Musalole kuti munthu wopusa azindinyoza.   Ndinakhala chete.Sindinatsegule pakamwa panga,+Chifukwa inu ndi amene munachita zimenezi.+ 10  Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera. Mphamvu zanga zatha chifukwa inu mwandipatsa chilango. 11  Mumathandiza munthu kuti asinthe pomupatsa chilango chifukwa cha zolakwa zake.+Mumawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete* imachitira. Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ (Selah) 12  Imvani pemphero langa, inu Yehova,Mvetserani pamene ndikulira kupempha thandizo.+ Musanyalanyaze misozi yanga. Chifukwa ndine mlendo kwa inu,+Mlendo wongodutsa mofanana ndi makolo anga onse.+ 13  Musandiyangʼane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalalaNdisanamwalire nʼkuiwalika.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “munatentha kwambiri.”
Kapena kuti, “Ndikuusa moyo.”
Kapena kuti, “kuti ndine wosakhalitsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amangopanga phokoso.”
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.