Salimo 40:1-17

  • Kuyamikira Mulungu amene palibe angafanane naye

    • Ntchito za Mulungu ndi zosawerengeka (5)

    • Mulungu sasangalala ndi nsembe zokha (6)

    • ‘Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna’ (8)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 40  Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,*Ndipo iye anatchera khutu* kwa ine nʼkumva kulira kwanga kopempha thandizo.+   Iye ananditulutsa mʼdzenje la madzi a mkokomo,Ananditulutsa mʼchithaphwi cha matope. Ndipo anapondetsa phazi langa pathanthwe,Anachititsa kuti ndiyende panthaka yolimba.   Kenako anaika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,+Nyimbo yotamanda Mulungu wathu. Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,Nʼkuyamba kukhulupirira Yehova.   Wosangalala ndi munthu amene amakhulupirira YehovaKomanso amene sadalira anthu otsutsa kapena anthu amene amakhulupirira mabodza.*   Inu Yehova Mulungu wanga,Mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa+Ndipo mumatiganizira.+ Palibe angafanane ndi inu.Nditati ndilankhule kapena kunena za zodabwitsazo,Zingakhale zochuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+   Nsembe zanyama komanso nsembe zina, simunazifune.*+Koma munatsegula makutu anga kuti ndimve.+ Simunapemphe nsembe zopsereza ndi nsembe zamachimo.+   Ndiyeno ine ndinati: “Taonani, ine ndabwera. Mumpukutu* munalembedwa za ine.+   Ndimasangalala* kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga,+Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+   Ndimalengeza uthenga wabwino wa chilungamo mumpingo waukulu.+ Onani! Sinditseka pakamwa panga,+Monga mmene mukudziwira, Inu Yehova. 10  Sindibisa chilungamo chanu mumtima mwanga. Ndimalengeza kuti ndinu wokhulupirika komanso kuti mumapulumutsa atumiki anu. Sindibisa chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu mumpingo waukulu.”+ 11  Inu Yehova, musasiye kundisonyeza chifundo. Chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu zizinditeteza nthawi zonse.+ 12  Masoka amene andizungulira ndi ambiri moti sindingathe kuwawerenga.+ Zolakwa zanga ndi zochuluka moti sindikutha kuona kumene ndikulowera.+Zachuluka kwambiri kuposa tsitsi lakumutu kwanga,Ndipo ndataya mtima. 13  Mukhale wofunitsitsa kundipulumutsa, inu Yehova.+ Ndithandizeni mofulumira, inu Yehova.+ 14  Onse amene akufuna kuchotsa moyo wangaAchititsidwe manyazi komanso anyozeke. Amene akusangalala ndi tsoka langaAbwerere mwamanyazi. 15  Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!” Achite mantha kwambiri chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zimene ziwachitikire. 16  Koma amene akufunafuna inu,+Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+ Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti: “Yehova alemekezeke.”+ 17  Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.Yehova aone zimene zikundichitikira. Inu ndi amene mumandithandiza komanso kundipulumutsa.+Inu Mulungu wanga, musachedwe.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “moleza mtima.”
Kapena kuti, “Ndipo iye anawerama kuti amvetsere.”
Kapena kuti, “anthu amabodza.”
Kapena kuti, “simunasangalale nazo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumpukutu wa buku.”
Kapena kuti, “Ndimafunitsitsa.”