Salimo 42:1-11

  • Kutamanda Mulungu yemwe ndi Mpulumutsi Wamkulu

    • Kulakalaka Mulungu ngati mmene mbawala imalakalakira madzi (1, 2)

    • “Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?” (5, 11)

    • “Yembekezera Mulungu” (5, 11)

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili* ya ana a Kora.+ 42  Mofanana ndi mbawala imene imalakalaka mitsinje ya madzi,Inenso* ndikulakalaka inu Mulungu.   Mofanana ndi munthu amene akulakalaka madzi, ndikulakalaka* Mulungu, Mulungu wamoyo.+ Ndidzapita liti kukaonekera pamaso pa Mulungu?*+   Misozi yanga ili ngati chakudya changa masana ndi usiku.Anthu amandinyoza tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+   Ndikukumbukira zinthu zimenezi ndipo mtima wanga ukupweteka kwambiri.Chifukwa poyamba ndinkayenda ndi gulu lalikulu la anthu,Ndinkayenda pangʼonopangʼono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,Gulu la anthu likuimba mosangalala nyimbo zoyamika Mulungu,Pa nthawi ya chikondwerero.+   Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima?+ Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga? Ndidzayembekezera Mulungu,+Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu.+   Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima.+ Nʼchifukwa chake ndakukumbukirani,+Pamene ndili mʼdziko la Yorodano ndi mʼmapiri a Herimoni,Pamene ndili mʼPhiri la Mizara.*   Madzi akuya akufuulira madzi akuyaKudzera mumkokomo wa mathithi anu. Mafunde anu onse amphamvu andimiza.+   Masana Yehova adzandisonyeza chikondi chake chokhulupirika,Ndipo usiku ndidzamuimbira nyimbo, ndidzapemphera kwa Mulungu amene amandipatsa moyo.+   Ndidzauza Mulungu, thanthwe langa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandiiwala?+ Kodi ndiziyenda wachisoni chifukwa chiyani? Nʼchifukwa chiyani adani anga akundipondereza?”+ 10  Anthu amene amadana nane kwambiri akundinyoza,*Amandinyoza tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+ 11  Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima? Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga? Ndidzayembekezera Mulungu,+Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu komanso Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Moyo wanga.”
Kapena kuti, “moyo wanga ukulakalaka.”
Apa akutanthauza kupita kunyumba ya Mulungu.
Kapena kuti, “phiri lalingʼono.”
Mabaibulo ena amati, “akundinyoza moti zikungokhala ngati akuphwanya mafupa anga.”