Salimo 43:1-5

  • Mulungu yemwe ndi Woweruza amapulumutsa

    • ‘Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu’ (3)

    • “Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?” (5)

    • “Yembekezera Mulungu” (5)

43  Ndiweruzeni inu Mulungu,+Nditetezeni pa mlandu wanga+ wotsutsana ndi mtundu wosakhulupirika. Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo komanso wochita zinthu zopanda chilungamo.   Inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+ Nʼchifukwa chiyani mwanditaya? Kodi ndiziyenda wachisoni chifukwa chiyani? Nʼchifukwa chiyani adani anga akundipondereza?+   Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+ Zimenezi zinditsogolere.+Zinditsogolere kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+   Kenako ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+Kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambiri. Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze+ inu Mulungu, Mulungu wanga.   Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima? Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga? Ndidzayembekezera Mulungu,+Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu komanso Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi