Salimo 44:1-26

  • Pemphero lopempha thandizo

    • “Ndi inu amene munatipulumutsa” (7)

    • Takhala ngati “nkhosa zokaphedwa” (22)

    • “Nyamukani kuti mutithandize!” (26)

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Masikili.* 44  Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,Makolo athu anatifotokozera+Ntchito zimene inu munachita mu nthawi yawo,Mʼmasiku akale.  2  Munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+Ndipo dziko lawo munalipereka kwa makolo athu.+ Munagonjetsa mitundu ya anthu nʼkuithamangitsa.+  3  Iwo sanatenge dzikolo pogwiritsa ntchito lupanga lawo.+Ndipo si mkono wawo umene unachititsa kuti apambane.+ Koma zimenezi zinatheka chifukwa cha dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,Chifukwa munkasangalala nawo.+  4  Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga.+Lamulani kuti Yakobo apambane.*  5  Ndi mphamvu zanu tidzathamangitsa adani athu.+Mʼdzina lanu tidzagonjetsa anthu amene akutiukira.+  6  Chifukwa sindidalira uta wanga,Ndipo lupanga langa silingandipulumutse.+  7  Ndi inu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+Ndi inu amene munachititsa manyazi anthu amene amadana nafe.  8  Tidzatamanda Mulungu tsiku lonse,Ndipo tidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale. (Selah)  9  Koma tsopano mwatitaya ndipo mwatichititsa manyazi,Simukutsogoleranso magulu athu ankhondo. 10  Mukuchititsa kuti tizithawa pamaso pa adani athu.+Anthu amene amadana nafe amatenga chilichonse chimene akufuna. 11  Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+ 12  Mwagulitsa anthu anu pamtengo wotsika kwambiri,+Ndipo simunapeze phindu pamalonda amenewo.* 13  Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azititonza,Komanso kuti anthu onse amene atizungulira azitinyoza ndi kutiseka. 14  Mwachititsa kuti anthu amitundu ina azitinyoza,*+Komanso kuti anthu azitipukusira mitu. 15  Ndimachita manyazi tsiku lonse,Ndipo nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi, 16  Chifukwa cha mawu a anthu amene akunditonza ndi kulankhula zachipongwe,Ndiponso chifukwa cha mdani wathu amene akufuna kutibwezera zoipa. 17  Zonsezi zatigwera, koma sitinakuiwaleni,Ndipo sitinaphwanye pangano lanu.+ 18  Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika,Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu. 19  Koma inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imakhala,Mwatiphimba ndi mdima wandiweyani. 20  Ngati tinaiwala dzina la Mulungu wathu,Kapena ngati tinapemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu, 21  Kodi Mulungu sakanadziwa zimenezi? Iye amadziwa zinsinsi zamumtima.+ 22  Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse.Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.+ 23  Dzukani. Nʼchifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+ Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+ 24  Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu? Nʼchifukwa chiyani mukuiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu? 25  Atigwetsera pafumbi.Matupi athu ali thasa! padothi.+ 26  Nyamukani kuti mutithandize+ Tipulumutseni* chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “alandire chipulumutso chachikulu.”
Kapena kuti, “pamtengo umenewo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti tikhale mwambi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tiwomboleni.”