Salimo 45:1-17

  • Ukwati wa mfumu yodzozedwa

    • Mawu osangalatsa (2)

    • “Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka muyaya” (6)

    • Mfumu idzalakalaka kukongola kwa mkwatibwi (11)

    • Ana anu adzakhala akalonga padziko lonse lapansi (16)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Salimo la ana a Kora. Masikili.*+ Nyimbo yachikondi. 45  Mtima wanga wasangalala kwambiri chifukwa cha nkhani yosangalatsa. Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za* mfumu.”+ Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera Malemba* waluso.+   Ndiwe wokongola kwambiri pakati pa ana a anthu. Mʼkamwa mwako mumatuluka mawu osangalatsa.+ Nʼchifukwa chake Mulungu wakudalitsa mpaka kalekale.+   Mangirira lupanga lako+ mʼchiuno mwako wamphamvu iwe,+Utavala ulemu ndiponso ulemerero.+   Upite mu ulemerero wako ndipo upambane.*+Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+Ndipo dzanja lako lamanja lidzachita* zinthu zochititsa mantha.   Mivi yako ndi yakuthwa ndipo ikuchititsa kuti anthu agwe pamaso pako.+Imalasa mitima ya adani a mfumu.+   Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka kalekale.+Ndodo ya ufumu wako ndi ndodo yachilungamo.+   Unkakonda chilungamo+ ndipo unkadana ndi zoipa.+ Nʼchifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, wakudzoza+ ndi mafuta achisangalalo+ chachikulu kuposa mafumu anzako.   Zovala zako zonse ndi zothiridwa mafuta onunkhira a mule, aloye ndi kasiya.*Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera mʼchinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.   Ana aakazi a mafumu ali mʼgulu la akazi amene umawalemekeza. Mkazi wamkulu wa mfumu waima* kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+ 10  Mvetsera, iwe mwana wanga wamkazi. Mvetsera mwatcheru ndipo utchere khutu.Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako. 11  Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,Chifukwa ndi mbuye wako,Choncho iweramire. 12  Mwana wamkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso.Amuna olemera kwambiri adzafuna kuti uwakomere mtima. 13  Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu mʼnyumba ya mfumu.Zovala zake ndi zokongoletsedwa* ndi golide. 14  Adzamubweretsa kwa mfumu atavala zovala zokongola.* Anamwali anzake omuperekeza akuwabweretsa kwa iwe. 15  Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.Ndipo adzalowa mʼnyumba ya mfumu. 16  Ana anu adzatenga malo a makolo anu, Ndipo mudzawaika kuti akhale akalonga padziko lonse lapansi.+ 17  Ndidzachititsa kuti anthu adziwe dzina lanu mʼmibadwo yonse yamʼtsogolo.+ Nʼchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ntchito zanga ndi zokhudza.”
Kapena kuti, “cha mlembi.”
Kapena kuti, “zikuyendere bwino.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakuphunzitsa.”
Kapena kuti, “Mfumukazi yaima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaziwombera limodzi ndi golide.”
Mabaibulo ena amati, “zovala zamaluwamaluwa.”