Salimo 48:1-14

  • Ziyoni ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu

    • Anthu padziko lonse amasangalala ndi phiri la Ziyoni (2)

    • Yenderani mzindawo ndi nsanja zake (11-13)

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 48  Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,Mumzinda wa Mulungu wathu, mʼphiri lake loyera.   Phiri la Ziyoni limene lili mʼdera lakutali lakumpoto,Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka komanso anthu padziko lonse lapansi akusangalala nalo,+Ndipo ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu.+   Munsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,Mulungu wasonyeza kuti iye ndi malo othawirako otetezeka.*+   Taonani! Mafumu asonkhana,*Onse pamodzi abwera.   Iwo ataona mzindawo, anadabwa. Anapanikizika nʼkuthawa mwamantha.   Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,Anavutika ngati mkazi amene akubereka.   Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu yakumʼmawa, munaswa sitima za ku Tarisi.   Zimene tinangomva, tsopano taziona tokha,Mumzinda wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ (Selah)   Inu Mulungu, ife timaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,+Tili mʼkachisi wanu. 10  Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu, mawu okutamandaniAfika kumalire a dziko lapansi.+ Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+ 11  Phiri la Ziyoni likondwere,+Matauni* a ku Yuda asangalale chifukwa cha zigamulo zanu.+ 12  Gubani mozungulira Ziyoni. Zungulirani mzinda wonsewo,Werengani nsanja zake.+ 13  Ganizirani mofatsa za mpanda wake wolimba.+ Yenderani nsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,Kuti mudzafotokozere mibadwo yamʼtsogolo. 14  Chifukwa Mulungu uyu ndi Mulungu wathu+ mpaka muyaya. Iye adzatitsogolera mpaka kalekale.*+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Kapena kuti, “anakumana atapangana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”
Mabaibulo ena amati, “kufikira imfa.”