Salimo 5:1-12

  • Yehova ndi malo othawirako a anthu olungama

    • Mulungu amadana ndi zoipa (4, 5)

    • “Ndinu wachilungamo, nditsogolereni” (8)

Kwa wotsogolera nyimbo pa Nehiloti.* Nyimbo ya Davide. 5  Mvetserani mawu anga inu Yehova,+Mvetserani mwatcheru kudandaula kwanga.   Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo,Inu Mfumu yanga komanso Mulungu wanga, chifukwa ndimapemphera kwa inu.   Inu Yehova, mʼmawa mudzamva mawu anga,+Mʼmawa ndidzafotokoza nkhawa zanga kwa inu+ ndipo ndidzadikira yankho lanu.   Chifukwa inu si Mulungu amene amasangalala ndi zoipa,+Palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu.+   Palibe anthu odzikuza amene angaime pamaso panu. Mumadana ndi anthu onse amene amachita zoipa.+   Mudzawononga anthu amene amalankhula mabodza.+ Yehova amadana ndi anthu achiwawa komanso achinyengo.*+   Koma ine ndidzalowa mʼnyumba yanu+ chifukwa cha chikondi chanu chachikulu komanso chokhulupirika.+Ndidzawerama nditayangʼana kumene kuli kachisi wanu wopatulika* chifukwa chokuopani.+   Inu Yehova ndinu wachilungamo,* nditsogolereni chifukwa adani anga andizungulira.Ndichotsereni zopunthwitsa mʼnjira yanu.+   Chifukwa palibe amene angakhulupirire chilichonse chimene anena.Mʼmitima yawo muli chidani chokhachokha.Mmero wawo ndi manda otseguka.Iwo amalankhula zachinyengo* ndi lilime lawo.+ 10  Koma Mulungu adzawapeza ndi mlandu.Adzagwa chifukwa cha ziwembu zawo zomwe.+ Muwathamangitse chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,Chifukwa iwo akupandukirani. 11  Koma anthu onse amene amathawira kwa inu adzasangalala.+Nthawi zonse adzafuula mosangalala. Inu mudzawateteza kuti anthu oipa asawafikire,Ndipo anthu okonda dzina lanu adzasangalala chifukwa cha inu. 12  Chifukwa inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.Mudzasangalala nawo ndipo mudzawateteza ndi chishango chachikulu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “munthu wokhetsa magazi ndi wachinyengo.”
Kapena kuti, “malo anu opatulika.”
Kapena kuti, “wolungama.”
Kapena kuti, “amalankhula zoshashalika.”