Salimo 50:1-23

  • Mulungu amaweruza okhulupirika ndi oipa

    • Kuchita pangano ndi Mulungu pogwiritsa ntchito nsembe (5)

    • “Mulungu ndi Woweruza” (6)

    • Nyama zonse ndi za Mulungu (10, 11)

    • Mulungu amaulula anthu oipa (16-21)

Nyimbo ya Asafu.+ 50  Yehova, Mulungu wa milungu+ walankhula.Iye akuitana anthu onse okhala padziko lapansi,Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.*   Mulungu wawala ali ku Ziyoni, mzinda wokongola kwambiri.+   Mulungu wathu adzabwera ndipo sangakhale chete.+ Pamaso pake pali moto wowononga,+Ndipo pamalo onse omuzungulira pali chimphepo chamkuntho.+   Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+Kuti aweruze anthu ake. Iye akuti:+   “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,Amene akuchita pangano ndi ine pogwiritsa ntchito nsembe.”+   Kumwamba kukulengeza kuti iye ndi wachilungamo,Chifukwa Mulungu ndi Woweruza.+ (Selah)   “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+ Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+   Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+   Sindikuyenera kutenga ngʼombe yamphongo mʼnyumba yanu,Kapena mbuzi* mʼmakola anu.+ 10  Chifukwa nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+Ngakhale nyama zopezeka mʼmapiri 1,000. 11  Ndikudziwa mbalame iliyonse ya mʼmapiri,+Nyama zosawerengeka zakutchire ndi zanga. 12  Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuzeni,Chifukwa dziko lonse ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi zanga.+ 13  Kodi ndiyenera kudya nyama ya ngʼombe zamphongoKapena kumwa magazi a mbuzi?+ 14  Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye,+Ndipo perekani kwa Wamʼmwambamwamba zimene mwalonjeza.+ 15  Pa nthawi yamavuto mundiitane.+ Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”+ 16  Koma Mulungu adzauza woipa kuti: “Ndi ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+Kapena wolankhula za pangano langa?+ 17  Iwe umadana ndi chilango,*Ndipo sumamvera mawu anga.*+ 18  Ukaona wakuba umasangalala ndi zochita zake.*+Ndipo umagwirizana ndi anthu achigololo. 19  Umagwiritsa ntchito pakamwa pako kufalitsa zinthu zoipa,Ndipo lilime lako limalankhula zachinyengo.+ 20  Umakhala pansi nʼkumanenera mʼbale wako zinthu zoipa,+Umaulula zolakwa za* mwana wamwamuna wa mayi ako. 21  Utachita zinthu zimenezi, ine sindinalankhule kanthu,Choncho unkaganiza kuti ndikuona zinthu ngati mmene iweyo ukuzionera. Koma tsopano ndikudzudzulaNdipo ndikuuza mlandu umene ndakupeza nawo.+ 22  Ganizirani zinthu zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani. 23  Amene akundiyamikira kuti ikhale nsembe imene akupereka kwa ine akundilemekeza.+Ndipo munthu amene akupitiriza kuchita zabwino,Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa mpaka kumadzulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuzi zamphongo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umaponya mawu anga kunkhongo.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mabaibulo ena amati, “umamutsatira.”
Kapena kuti, “Umaipitsa mbiri ya.”