Salimo 53:1-6

  • Zimene anthu opusa amachita

    • “Kulibe Yehova” (1)

    • “Palibe aliyense amene akuchita zabwino” (3)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe potsatira kaimbidwe ka Mahalati.* Masikili.* Salimo la Davide. 53  Munthu wopusa* amanena mumtima mwake kuti: “Kulibe Yehova.”+ Zochita zopanda chilungamo za anthu amenewa ndi zoipa komanso zonyansa,Ndipo palibe amene akuchita zabwino.+   Koma kuchokera kumwamba, Mulungu amayangʼana ana a anthu,+Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, ngati pali aliyense amene akufunafuna Yehova.+   Onse apatuka,Ndipo onsewo ndi achinyengo. Palibe aliyense amene akuchita zabwino,Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+   Kodi palibe aliyense womvetsa zinthu pakati pa anthu ochita zoipawa? Iwo amadya anthu anga ngati kuti akudya chakudya. Ndipo sapemphera kwa Yehova.+   Koma adzagwidwa ndi mantha aakulu,Mantha amene sanayambe agwidwapo chiyambire,*Chifukwa Mulungu adzamwaza mafupa a anthu amene akukuukirani.* Mudzawachititsa manyazi chifukwa Yehova wawakana.   Zikanakhala bwino chipulumutso cha Isiraeli chikanachokera ku Ziyoni.+ Yehova akadzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wopanda nzeru.”
Mabaibulo ena amati, “Adzachita mantha popanda chochititsa mantha chilichonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amanga msasa kuti akuukireni.”