Salimo 54:1-7
-
Pemphero lopempha kuthandizidwa pa nthawi youkiridwa ndi adani
-
“Mulungu ndi amene amandithandiza” (4)
-
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene amuna a ku Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Davide akubisala kwathu.”+
54 Inu Mulungu, ndipulumutseni mʼdzina lanu,+Ndipo nditetezeni*+ ndi mphamvu zanu.
2 Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+Tcherani khutu ku mawu ochokera mʼkamwa mwanga.
3 Chifukwa anthu achilendo andiukira,Ndipo anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga.+
Iwo salemekeza Mulungu.*+ (Selah)
4 Taonani! Mulungu ndi amene amandithandiza.+Yehova amadalitsa anthu amene akundithandiza.
5 Iye adzabwezera adani anga+ zoipa zimene akuchitira anthu ena.Inu Mulungu wanga, awonongeni* chifukwa ndinu wokhulupirika.+
6 Ndidzapereka nsembe kwa inu+ mofunitsitsa.
Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu chifukwa ndi labwino.+
7 Inu mumandipulumutsa pa mavuto anga onse,+Ndipo ndidzayangʼana adani anga atagonja.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ndiikireni kumbuyo pa mlandu wanga.”
^ Kapena kuti, “Iwo saika Mulungu patsogolo pawo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “akhalitseni chete.”