Salimo 57:1-11

  • Kupempha kuchitiridwa chifundo

    • Kuthawira pansi pa mapiko a Mulungu (1)

    • Adani adzagwera mumsampha wawo womwe (6)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli nʼkukalowa mʼphanga.+ 57  Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,Chifukwa ine ndathawira kwa inu.+Ndathawira mumthunzi wa mapiko anu mpaka mavuto atadutsa.+   Ndikufuulira Mulungu Wamʼmwambamwamba,Mulungu woona amene akuthetsa mavuto amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.   Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba nʼkundipulumutsa.+ Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake. (Selah) Mulungu adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika ndi choonadi chake.+   Ndazunguliridwa ndi mikango.+Ndikuyenera kugona pakati pa anthu amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+   Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+   Iwo atchera ukonde kuti akole mapazi anga.+Ndili ndi nkhawa yaikulu.+ Anakumba dzenje panjira yanga,Koma agweramo okha.+ (Selah)   Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu,+Ndatsimikiza mtima. Ndidzakuimbirani nyimbo ndi zipangizo zoimbira.   Dzuka, iwe ulemerero wanga. Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze. Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.+   Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+ 10  Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo. 11  Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+

Mawu a M'munsi