Salimo 58:1-11

  • Pali Mulungu amene amaweruza dziko lapansi

    • Pemphero lopempha kuti anthu oipa alangidwe (6-8)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* 58  Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+ Kodi mungaweruze mwachilungamo, inu ana a anthu?+   Ayi, mʼmalomwake mukuganiza zochita zinthu zopanda chilungamo mumtima mwanu,+Ndipo mumalimbikitsa zachiwawa mʼdzikoli.+   Oipa amasochera* akangobadwa.*Iwo amakhala osamvera komanso abodza kuchokera nthawi imene anabadwa.   Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka.+Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake.   Singamve mawu a anthu amatsenga,Ngakhale atachita matsengawo mwaluso.   Inu Mulungu, agululeni mano mʼkamwa mwawo. Inu Yehova, thyolani nsagwada za mikango* imeneyi.   Asowe ngati madzi amene akuyenda. Mulungu akoke uta wake nʼkuwagwetsa ndi mivi yake.   Akhale ngati nkhono imene imasungunuka ikamayenda.Ngati mwana wa mayi amene wapita padera, yemwe saona dzuwa.   Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,Mulungu adzauluza mitengo yaiwisi komanso imene ikuyaka ngati ikuuluzika ndi mphepo yamkuntho.+ 10  Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+Mapazi ake adzaponda magazi a anthu oipa.+ 11  Kenako anthu adzati: “Ndithudi wolungama amalandira mphoto.+ Ndithudi pali Mulungu amene amaweruza padziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amachita zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”