Salimo 59:1-17

  • Mulungu ndi chishango komanso malo othawirako

    • ‘Musasonyeze chifundo kwa anthu achiwembu’ (5)

    • “Ndidzaimba za mphamvu zanu” (16)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu kukadikirira nyumba yake kuti amuphe.+ 59  Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni kwa adani anga.+Nditetezeni kwa anthu amene akundiukira.+   Ndilanditseni kwa anthu ochita zoipa,Ndipo ndipulumutseni kwa anthu achiwawa.*   Inu Yehova, taonani! Iwo amandidikirira panjira.+Anthu amphamvu amandiukiraKoma osati chifukwa chakuti ndapanduka kapena kuchita tchimo lililonse.+   Ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse, iwo akuthamanga ndipo akukonzekera kundiukira. Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.   Chifukwa inu Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+ Nyamukani ndipo muone zimene mitundu yonse ya anthu ikuchita. Musasonyeze chifundo kwa aliyense woipa komanso wachiwembu.+ (Selah)   Amabwera madzulo aliwonse.+Amauwa ngati agalu+ ndipo amazungulira mzinda wonse.+   Tamverani zimene zikutuluka pakamwa pawo.Milomo yawo ili ngati malupanga,+Chifukwa iwo akuti: “Ndani akumvetsera?”+   Koma inu Yehova, mudzawaseka.+Mudzanyoza mitundu yonse ya anthu.+   Inu Mphamvu yanga, ndidzayangʼanabe kwa inu.+Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka.*+ 10  Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika adzandithandiza.+Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga atagonja.+ 11  Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga asaiwale. Ndi mphamvu zanu achititseni kuti aziyendayenda,Achititseni kuti agwe, inu Yehova, chishango chathu.+ 12  Chifukwa cha tchimo lapakamwa pawo ndi mawu a milomo yawo,Ndiponso chifukwa cha mawu otukwana komanso achinyengo amene amalankhula,+Akodwe ndi kunyada kwawoko. 13  Muwawononge onse mutakwiya.+Muwawononge kuti asakhaleponso.Muwadziwitse kuti Mulungu akulamulira mbadwa za Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ (Selah) 14  Asiyeni abwerenso madzulo.Asiyeni auwe ngati agalu ndipo azizungulira mzinda wonse.+ 15  Asiyeni aziyendayenda kufunafuna chakudya.+Musalole kuti akhute kapena kupeza malo ogona. 16  Koma ine, ndidzaimba za mphamvu zanu.+Mʼmawa ndidzanena mosangalala za chikondi chanu chokhulupirika. Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako otetezeka,+Ndiponso malo anga othawirako pa nthawi ya mavuto.+ 17  Inu Mphamvu yanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani,+Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka, Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ofunitsitsa kukhetsa magazi.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”