Salimo 6:1-10
Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,Musandilangize mutapsa mtima.+
2 Ndikomereni mtima,* inu Yehova, chifukwa ndayamba kufooka.
Ndichiritseni, inu Yehova,+ chifukwa mafupa anga akunjenjemera.
3 Ine ndasokonezeka* kwambiri,+Ndipo ndikufunseni, inu Yehova, kodi ndipitiriza kuvutika mpaka liti?+
4 Bwererani, inu Yehova, mudzandipulumutse.+Ndipulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+
5 Chifukwa akufa satchula* za inu.Kodi ndi ndani amene angakutamandeni ali mʼManda?*+
6 Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga.+Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa* ndi misozi,Ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.+
7 Maso anga afooka chifukwa cha chisoni changa.+Maso anga achita mdima* chifukwa cha anthu onse amene akundizunza.
8 Ndichokereni pamaso panga inu nonse amene mumachita zoipa,Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.+
9 Yehova adzamva pempho langa loti andikomere mtima.+Yehova adzayankha pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzataya mtima.Iwo adzathawa mwadzidzidzi komanso mwamanyazi.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Ndichitireni chifundo.”
^ Kapena kuti, “Moyo wanga wasokonezeka.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “sakumbukira.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimapangitsa kuti bedi langa liyandame.”
^ Kapena kuti, “akalamba.”