Salimo 60:1-12

  • Mulungu amagonjetsa adani

    • Chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake (11)

    • “Mulungu adzatipatsa mphamvu” (12)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo ya “Duwa la Chikumbutso.” Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira. Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera nʼkukapha Aedomu 12,000 mʼchigwa cha Mchere.+ 60  Inu Mulungu, munatikana ndipo munatigonjetsa.+ Munatikwiyira. Koma tsopano tiloleni tibwerere kwa inu.   Mwachititsa kuti dziko lapansi ligwedezeke ndipo mwalingʼamba. Tsekani mingʼalu yake, chifukwa likugwa.   Mwachititsa kuti anthu anu akumane ndi mavuto. Mwatimwetsa vinyo amene wachititsa kuti tiziyenda dzandidzandi.+   Perekani* chizindikiro kwa anthu amene amakuopaniKuti athawe ndi kuzemba uta. (Selah)   Kuti anthu amene mumawakonda apulumutsidwe,Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutiyankhe.+   Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti: “Ndidzasangalala popereka Sekemu ngati cholowa,+Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+   Giliyadi ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,+Ndipo Efuraimu ndi chipewa choteteza* mutu wanga.Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+   Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+ Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+ Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+   Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wozunguliridwa ndi adani?* Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+ 10  Kodi si inu Mulungu amene munatikana,Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+ 11  Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+ 12  Mulungu adzatipatsa mphamvu,+Ndipo adzapondaponda adani athu.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Mwapatsa.”
Mabaibulo ena amati, “Mʼmalo ake opatulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo achitetezo oteteza.”
Mabaibulo ena amati, “wotetezedwa.”