Salimo 61:1-8

  • Mulungu ndi nsanja yolimba imene imateteza kwa adani

    • “Ndidzakhala mlendo mutenti yanu” (4)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide. 61  Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kopempha thandizo. Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+   Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi ndidzafuulira inuPamene mtima wanga walefuka.*+ Nditsogolereni nʼkundikweza pathanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+   Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako,Nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.+   Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.+Ndidzabisala mumthunzi wa mapiko anu.+ (Selah)   Chifukwa inu Mulungu, mwamva malonjezo anga. Mwandipatsa cholowa chimene ndi cha anthu amene amaopa dzina lanu.+   Mudzatalikitsa moyo wa mfumu,*+Ndipo idzakhala ndi moyo ku mibadwomibadwo.   Mfumuyo idzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale pamaso pa Mulungu.+Chikondi chanu chokhulupirika komanso kukhulupirika kwanu ziiteteze.+   Mukatero ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka kalekale,+Pamene ndikukwaniritsa malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “uli ndi nkhawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku a mfumu.”